Kuno ku namiyango mseu wathu sulibwino ayi. achitepo kanthu
Ndati ndipemphe nawo kuti mseu wopita ku Mtunda ku Area 25C New vision suli bwino ngati kungatheke atithilireko dothi
Pempho langa kuno ku Machinjiri ndi lakuti atikonzere miseu ingapo monga wochoka pa Khama to Chikoti market
Ndati ndipemphe nawo kudzera mwa Khansala wathu kuti mseu wochoka pa Khama to miseu 6 sulibwino. Atiganizire pa malingaliro awo achitukuko mtsogolo muno
Miseu yaonongeka maka Ku nandolo ndi Ku mboni.
Kuno ku Masasa ward Mzuzu tikuwonga Khansala withu Yona Mkandawire pakutinozgera ulalo pa Chideso.
I wish to reach out to the Councilor for Limbe ward to take the initiative to undertake maintenance work on the foot-pass bridges that connect Limbe market to the upper area where there are shops.
Kuno kwa Chinsapo 2 tingasangalare atatikonzera nsewu wochoko pa Chinangwa kupita pa sukulu ya Kakule primary
Ine m'malo mwa anzanga ena kuno kwa Senti tili osakhutira ndi m'mene nseu waukulu kuno wakonzedwera. Mbali zina zomwe amaliza kale kukonza kuno zayamba kale ma pothole sitikudziwa kuti kodi ndi ukatswiri omwe unachepa kapena material sidali yokwanira
Kuno ku Makata Blantyre mlatho wa pa mtsinje wa Mlombozi suli bwino udaonongeka ndi mvula. Uthenga tidaufikitsa kale kwa atsogoleri ndipo tikukhulupilira kuti ngakhale iwo eni ake akudziwa koma sitidamveko ndi lonjezo limene loti achitapo kanthu
I would like to report that the M1 road has completely been cut off at Jalawe in Rumphi. Vehicles from Mzuzu or Karonga are using a road that cuts through Mchenga Coal Mine and Ntchenachena to Phwezi.
Tikuwonga Councillor withu kuno ku Zolozolo East pakuti zengera Bridge pa kuya pa Zolozolo primary School.