mukunena miseu yonse kapena umodzi? ndipo para niumodzi uli mwa blockleader njani? Stafford Khunga - Khansala
Ndikupempha ngati kuli kotheka pa mjirijiri butchery tikamapita pa 4ways ya king shaka bar bridge linabooka komanso tikamapita ku ching'ambo from up chiputula primary pafupi ndi seventhday church. andrew chavula concerned citizen
Tati tipemphe nawo kuti Khansala wathu kuno ku Zolozolo east atikonzere nseu wa kwa BagiDadi
Kuno kwa T/A Makata ku Blantyre, bridge ya pa mtsinje wa Mlombozi inakokoloka chaka chatha,koma mpakana pano sunakonzedwe. Tiyembekezere kuti ukonzedwa liti,chifukwa nyengo yamvula ndiye yafikanso
Tati tipemphe nawo kudzera pa Mzinda kuti atithandize kuno kwa Jokala ku Zomba, nkhani ya mseu, mseu wathu kuno sulibwino. Matias Kalemba
Chonde brige yolumikiza area 36 ndi tumbwe,payelea ndi kupita kwamitengo,akufuna padzafe kaye munthu? nafenso anthu khalidwe loba mitengo silabwino. Hardson Lefan.champhepete village (area 36,LL).
Ine ndim'nyamata ochokela ku chiladzulu south,koma khawa zanga zili pa khansala wanthu naphiyo,pali mulatho wachimwawa umene walumikiza mafumu awili,asakwata komaso mangulama mulatho wapakati pamafumu awili amenewa sulibwino konse,moti sindikudziwa ngati phungu wadela limeneli amene ali josefe mwanamvekha akudziwa zamavuto amenewa,mwachidule inu a Mzinda tapitani kuchiladzulu south kwa t/a nkalo mudzi mwamatope,siliya,ngoniwa,misomali,sakwata,mangulama,mwamidzi yochepa chabe muone mabvuto,ndimakuvetsesani ndim'mene mumapangila kapena kufufuzila zinthu, ine dzinalanga ndi evans mpethela namuku
In Zolozolo West; the road from CCAP through Bagidadi area needs upgrading. We engaged our councilor before and we were told that it is amongst the roads for consideration under the MASAF project but we don’t know when.
Kuno ku mamiyango vuto ndi madzi ndi magetsi komanso miseu silibwino
Kuno kunamiyango tikupempha nawo nseu watala ngati anzathu ku Mthandizi
Kuno ku Chiputula ku Mzuzu mseu suli bwino. Tipemphe nawo khansala wathu kuti atithandize