Zolozolo East ward kuli vuto la milatho moti ana akumavutika kuoloka kuti apite pa Zolozolo primary school
Kuno ku Kasungu msewu womwe unaonongeka ma yenje ayamba kuukonza
Kuno kwathu program yokonza miseu yidaimila panjira monga mseu wa kwa Senya to Chitete river ndi Kapindula to Chitete. Sitikudziwa kuti asembule ma plan awo ndiotani
Balaka Shire ward umbava wavuta ku Mwima. Every week kumapezeka shop yabedwa
Ku Masakapende kuli vuto la bridge yomwe inaphotchoka kale kale koma siyikukonzedwa
Chipatala cha Mwima chatha zaka 17 koma osachitsegulila. Anthu adandaula koma kuli zii
Kuno ku Kasungu misika yambiri ing'onoing'ono mulibe ma toilet koma ma tiketi timaduladaily. Kodi ndalamazo zimagwira ntchito yanji
Ngalande za mu msika ndi zosafukula kuno ku Kasungu chinthu chomwe chikupangisa kuti madzi azilowa pamalo ogulitsira malonda
Kasungu West kwa Sub-TA Mawawa, kodi boma bwanji likupereka zithu zochepa pazipangizo zomwe adalonjeza? Ndalama ya labor K50,000 sakutipatsa, ma door frame ndi mawindow sakutipatsa. kodi nanga ngongoleyi tizabweza bwanji ngati katundu wina sititenga
Ine ndimakhala ku zingwangwa ku BT, ndimati ndidandaule miseu yathu mu dela limeneli siili bwino. Maenje maenje ndithu ndiye madzi a mvula akumadikha mmenemu, sizili bwino ndithu
Njala yafika povuta ku balaka makamaka dela la Mfumu yaikulu Phimbi pomwe anthu anayi sabata yatha anakomoka ndi njala zomwe zapangitsa phungu wa delali Ireen Mambala kugawa chakudya kwa ena mu delali
Kusatuluka kwa madzi mmalo ena oyandikira pa town assembly kuno ku Kasungu kukweza chiophyeza chakufala kwa matenda odza Kamba ka Ntchetche
vuto la nseu kuno ku ngerenge karonga. wadyeka kwambiri magalimoto akulephera kudusa
Kuno ku Balaka Central East kagawidwe ka chimanga sikakuyenda bwino, ma khansala and akulu akulu azipani kumadera akumangoba thandizolo likabwera
Kuno ku Kasungu Chitetezo chachepa anthu akumalanga okha akuba. chonde tithandizeni