Kwathu kuno katundu akubedwa.. anthu akuphedwa paliibe chabwino kukacha timamva nkhani za chisoni ........ a MP anthu tinawafotokozela kuti kuta khala police station bola tithandizika....... anangoti amva
kuno kwathu ku chingale Zomba mlatho unakokoloka a MP anthu sitinawauze chifukwa amafika kuno nthawi ya campaign ... pano amakhala ku town tilibe angatithandize
Kwathu kuno mbali mwa nseu mulibe magetsi a MP anthu tinawauza koma mpaka lero sakuchitapo kathu
Nseu wa ku ma puloti suli bwino kukagwa mvula timavutika chifukwa cha matope ma galimoto amavutika kuyenda, nazo njinga sitimayendesa chifuka cha ku telela kwa mu nseu....tinawauza a MP anthu koma anangobweletsa nchenga komano ntchito siyinayambike
Kwathu kuno magetsi sakuyaka tikutha 1 week pano wopanda magetsi kuwauza a-Escom faults anangoti amva pali vuto la transformer.
ku bangwe madzi akuvuta mwezi uno wachitatu tidaona kuti patokha mpovuta kepereka dandaulo ku Water Board nde tidakamba ndi bwana MP anangoti atithandiza mpaka pano
Kuno kwathu miseu silibwino. tufuna langizo kuti tingasate bwino m'mene ndalama zokonzera mseu zidagwirira ntchito
Here in zomba at kalinde, there is a broken sewage pipeline that causes bad smell in our city.We talked to the counselors but they are not helping.
kuno Kwathu ku Dedza pa Chimbiya kulibe nseu wolongosoka kupita ku St Kizito tinawafotokozela a MP anthu ndipo anati atithandiza ndee maso anthu ali ku njira kuyang'anira kwa MP