Ndati ndifikire ndi uthenga kwa Khansala wathu ndinso mafumu kuno ku Nyama ward kwa Kauma kuti achitepo kanthu pa khalidwe la anthu omwe amaunjika zinyalala m'masaka nkumalawira usiku mobisa kukataya malo osayenera.
Kuno ku Nkolokoti ward ku Blantyre ena mwa mavuto omwe tili nawo ndi akuti ma bin omwe adatipasa m'misika akuchepa kotero anthu akungotaya zinyalala mu mtsinje ndi malo ena osayenerera komanso miseu yathu siyolongosoka
Ine ndati ndiwafikire nawo uthenga woyamba olemekezeka bambo Litchowa omwe apambana pa ukhansala kuno ku Ndirande Makata. Tikudziwa ntchito si yawo yokha ndipo akuyenera kugwira limodzi ndi Phungu ndinso kukhonsolo koma alingalire izi: 1. Pa sukulu ya Makata ma toilet okwanira palibe 2. Pa msika wa Makata pakufunika chi bin chotayilamo zinyalala. 3. Miseu yomwe idalowa mkati yambiri silibwino. Atipemphereko kuti azapale monga adapangira ku madera ena ngati Bangwe
Zinyalala zochuluka zili pansi ndipo bin yazaza pa msika wa pa Khama. Therefore we ask the city council to assist us. Here in Nkolokoti ward.
Chilobwe market pano patha ma sabata awiri osesa mu msika akukhonsolo asakusesa chonsecho ndalama yapangira malonda mu msika akutidula
pa msundwe market palibe ma toilet okwanira
Kuno ku Namitete pempho atikonzere mseu wopita pa msika
Pa msika wa Mathambi pakuchepa anthu osesa. Panopa alipo mmodzi yekha ndipo lero wadwala kotero sabata yonseyi simunasesedwe.
LLCH 1 Kuno ku Chigwirizano market pempho lathu ndi lakuti azachose dzala pomwe tikutayapo pano likupereka chiophyezo cha matenda. Lisunthire pena olo atipase Bin yaikulu
Waste has accumulated badly at the bin site at Mwenyekondo market close to Msonkhamanja CCAP. Its been 5 days now. Please assist.
Kuno ku Blantyte Chilobwe market. Osesa mu nsika achilimike. magawo ena amsika monga kwa amayi ogulitsa tomato amalekelera zinyalala ziunjikane
Ndati ndifikire ndi uthenga kwa Khansala wathu ndinso mafumu kuno ku Nyama ward kwa Kauma kuti achitepo kanthu pa khalidwe la anthu omwe amaunjika zinyalala m'masaka nkumalawira usiku mobisa kukataya malo osayenera. izizi ndizotiso zitha kudzesa matenda.